Chikhulupiliro Cha Moyo: Zomwe Anazarene Amakhulupilira

Chikhulupiliro Cha Moyo: Zomwe Anazarene Amakhulupilira

Chikhulupiliro Cha Moyo

Zomwe Hnazarene Amakhulupilita

Bungwe lina lililonse limene lakhala nthawi yaitali likugwira ntchito zake molimbika, limakhoza kukhazikitsidwa kuti lidzigwirira ntchito pamodzi ndi mabungwe ena, pofuna kukwaniritsa cholinga cha bungwelo pothandiza mabungwe enawo kuti naonso atukuke. M’menemu ndi m’mene ulilinso Mpingo wa Nazarene. Iwo unapangidwa kudzasintha dziko lapansi pakufalitsa uthenga wa chiyeretso cha m’mawu a Mulungu. Mpingo waukuluwu ndi umene unakhazikitsidwa kukhala wachiyeretso mu nthawi yomweyo. Utumiki wathu ndi kupanga ophunzira kukhala monga Khristu ku mafuko onse.

Moyo watsopano ndi tsogolo la Mpingo wa Nazarene umafotokozedwa ndi kutenga mbali mu utumiki wa Mulungu. Choncho ndi chifanizo cha mpingo wa Khristu Yesu ndi bungwe limene linapangidwa lofunikira osangoti pa zimene limakhulupilira koma m’mene limachitira pakuikira ndemanga za Ufumu wa Mulungu wokha basi.

Pamene Mpingo wa Nazarene ukulowa mu zaka zina chikwi zatsopano (2000A.D.), ndikoyenera kuzindikira zinthu izi zoonekeratu zapadera zimene tazivomereza ndikusangalala mwachimwemwe. Chuma chathu chofunikira kwambiri ndi -utumiki, maitanidwe, zikhulupiliro ndi zofunika zathu zapamwamba - tikuzipereka mokondwa ngati mphatso ku mibadwo imene ili nkudza.

Tikupemphera kuti zinthu zofunika zimene ife takhazikikamo kuti zidzapitirira kutumikira monga muuni wotsogolera kwa iwo amene akufunika kuyenda mkuwala ndi mu mthunzi wa zaka zimene zili kutsogolo.

Zinthu Zofonika Zomwe Takhazikikamo

1. Ndife Anthu Achikhristu

Monga Akhristu a mpingo woona, timagwirizana ndi okhulupilira onse pakudziwitsa anthu za Umbuye wa Yesu Khristu ndiko kuvomereza mfundo ya chikhulupiliro cha chikhristu ya Mulungu m’modzi mwa atatu. Timalemekeza kwambiri chiyero chimene chinayambitsidwa kalekale ndi a Wesley ndipo timakhulupilira kuti ndi njira yakumvetsetsa bwino chikhulupiliro chimene chili choona m’malembo, m’malingaliro, m’chikhalidwe ndi mkakhalidwe kake.

2. Ndife Anthu Achiyero

Mulungu amene ali woyera, akutiitana ife ku moyo umene uli wa chiyero. Timakhulupilira kuti Mzimu Woyera amafuna kuchita ntchito yachiwiri ya chisomo, imene imatchulidwa mu maunso ena monga ‘kuyeretsedwa kwathunthu’ ndi ‘kubatizidwa ndi Mzimu Woyera’ kutiyeretsa ife ku machimo onse: kutikonzanso mwatsopano m’chifanizo cha Mulungu: kutilimbikitsa ife kumkonda Mulungu ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, maganizo athu onse ndi mphamvu zathu zonse ndi anzathu onse monga m’mene ife tidzikondera ife eni.

3. Ndife Anthu Otumidwa

Ndife anthu otumidwa amene tavomera kuitana kwa Khristu ndi opatsidwa mphamvu ndi Mzimu Woyera kupita m’dziko lapansi, ndikuchita umboni za Khristu Ambuye ndi kutengapo mbali ndi Mulungu pomanga mpingo ndi kukulitsa ufumu wake (2 Akorinto 6:1). Utumiki wathu: (a) Umayamba pakupembedzera; (b) Pakulalikira kwa anthu kudzera mukukopa anthu kuti abwere kwa Yesu ndiponso muzachifundo; (c) Pakulimbikitsa okhulupilira kuti akhwime mu chikhristu kudzera m'maphunziro a ophunzira; (d) Pakukonzekeretsa amayi ndi abambo ku ntchito ya chikhristu kudzera mu maphunziro apamwamba.

Tabs